Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 23:18-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19. Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? cifukwa cace anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.

20. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;

21. ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22. Izi anacita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23. Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ace.

24. Asaheli mbale wa Yoabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25. Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26. Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekoi.

27. Abiyezeri M-anetori, Mebunai Mhusati;

28. Zalimoni M-ahohi, Maharai Mnefati;

29. Helebi mwana wa Baana Mnetofati, ltai mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa ana a Benjamini;

30. Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31. Abialiboni M-aribati, Azmaveti Mbahurimi;

32. Eliaba Mshaliboni wa ana a Jaseni, Jonatani;

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 23