Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 20:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tiribe gawo mwa Davide, tiribenso colowa mwa mwana wa Jese; munthu yense apite ku mahema ace, Israyeli inu.

2. Comweco anthu onse a Israyeli analeka kutsata Davide, natsata Seba mwana wa Bikri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordano kufikira ku Yerusalemu.

3. Ndipo Davide anafika kunyumba kwace ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa cakudya, koma sanalowana nao. Comweco iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

4. Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 20