Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tiribe gawo mwa Davide, tiribenso colowa mwa mwana wa Jese; munthu yense apite ku mahema ace, Israyeli inu.