Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 2:26-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Pomwepo Abineri anaitana Yoabu nati, Kodi lupanga lidzaononga cionongere? sudziwa kodi kuti kutha kwace kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?

27. Yoabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapandakunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wace.

28. Comweco Yoabu anaomba Gpenga, anthu onse naima, naleka kupitikitsa Aisrayeli, osaponyana naonso.

29. Ndipo Abineri ndi anthu ace anacezera usiku wonse kupyola cidikha, naoloka Yordano, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu.

30. Ndipo Yoabu anabwerera pakutsata Abineri. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asaheli.

31. Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abineri, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi.

32. Ndipo ananyamula Asaheli namuika m'manda a atate wace ali ku Betelehemu. Ndipo Yoabu ndi anthu ace anacezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawacera ku Hebroni.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 2