Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.

21. Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simeyi cifukwa ca kutemberera wodzozedwa wa Yehova?

22. Koma Davide anati, Ndiri ndi ciani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israyeli lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israyeli lero?

23. Ndipo mfumu inanena ndi Simeyi, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.

24. Ndipo Mefiboseti mwana wa Sauli anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ace, kapena kumeta ndebvu zace, kapena kutsuka zobvalazace kuyambira tsiku lomuka mfumukufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.

25. Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Cifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?

26. Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19