Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 17:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;

2. ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofoka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;

3. ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere.

4. Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akuru onse a Israyeli.

5. Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai M-ariki yemwe, timvenso cimene anene iye.

6. Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofeli analankhula mau akuti; ticite kodi monga mwa kunena kwace? ngati iai, unene ndiwe.

7. Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofeli suli wabwino.

8. Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ace kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga cimbalangondo cocilanda ana ace kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.

9. Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, ali yense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.

10. Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wace ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisrayeli onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 17