Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 11:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsildra ku nyumba yace, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? cifukwa ninji sunatsikira ku nyumba yako?

11. Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israyeli, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yoahu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi ku nyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzacita cinthuci.

12. Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pane leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke, Comweco Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwace.

13. Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pace; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anaturuka kukagona pa kama wace pamodzi ndi anyamata a mbuye wace; koma sanatsildra ku nyumba yace.

14. Ndipo m'mawa Davide analembera Yoabu kalata, wopita nave Uriya.

15. Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.

16. Ndipo Yoabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriye pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.

17. Ndipo akumudziwo anaturuka, namenyana ndi Yoabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Mhiti anafanso.

18. Pamenepo Yoabu anatumiza munthu nauza Davide zonse za nkhondoyi;

19. nauza mthengawo kuti, Utatsiriza kuuza mfumu zonse za nkhondozo;

20. kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Cifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamudzi kukamenyana nao? Simunadziwa kodi kuti apalingawo adzaponya?

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 11