Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 1:10-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. M'mwemo ndinakhala pambali pace ndi kumtsiriza cifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wace, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pace, ndi cigwinjiri ca pa mkono wace, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

11. Pomwepo Davide anagwira zobvala zace nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.

12. Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, cifukwa ca Sauli ndi mwana wace Jonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israyeli, cifukwa adagwa ndi lupanga.

13. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, M-amaleki.

14. Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaopa kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?

15. Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe, Ndipo anamkantha, nafa iye.

16. Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; cifukwa pakamwa pako padacita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.

17. Ndipo Davide analirira Sauli ndi Jonatani mwana wace ndi nyimbo iyi ya maliro;

18. nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Jasari:-

19. Ulemerero wako, Israyeli, unaphedwa pa misanje yako.Ha! adagwa amphamvu

20. Usacinene ku Gati,Usacibukitse m'makwalala a Asikeloni,Kuti ana akazi a Afilisti angasekere,Kuti ana akazi a osadulidwawo angapfuule mokondwera.

21. Mapiri inu a Giliboa,Pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka.Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,Cikopa ca Sauli, monga ca wosadzozedwa ndi mafuta.

22. Uta wa Jonatani sunabwerera,Ndipo lupanga la Sauli silinabwecera cabe,Pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

23. Sauli ndi Jonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao,Ndipo m'imfa yao sanasiyana; Anali nalo liwiro loposa ciombankanga,Anali amphamvu koposa mikango.

24. Ana akazi inu a Israyeli, mulirire Sauli,Amene anakubvekani ndi zofira zokometsetsa,Amene anaika zokometsetsa zagolidi pa zobvala zanu.

25. Ha! amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo!Jonatani anaphedwa pamisanje pako.

26. Ndipsinjika mtima cifukwa ca iwe, mbale wanga Jonatani;Wandikomera kwambiri;Cikondi cako, ndinadabwa naco,Cinaposa cikondi ca anthu akazi.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 1