Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 36:21-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ace; masiku onse a kupasuka kwace linasunga sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.

22. Caka coyamba tsono ca Koresi mfumu ya Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,

23. Atero Koresi mfumu ya Perisiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Ali yense mwa inu a anthu ace onse, Yehova Mulungu wace akhale naye, akwereko.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 36