Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 36:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zace zonse zacifumu ndi moto, naononga zipangizo zace zonse zokoma.

20. Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babulo, nakhala iwo anyamata ace, ndi a ana ace, mpaka mfumu ya Perisiya idacita ufumu;

21. kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ace; masiku onse a kupasuka kwace linasunga sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.

22. Caka coyamba tsono ca Koresi mfumu ya Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 36