Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 35:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israyeli, ndi umo adalembera Solomo mwana wace.

5. Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.

6. Ndipo muphere Paskha, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kucita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.

7. Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, ana a nkhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paskha kwa ali yense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa cuma ca mfumu.

8. Ndi akulu ace anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehieli, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paskha.

9. Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netaneli, abale ace, ndi Hasabiya, ndi Yeyeli, ndi Yosabadi, akuru a Alevi, ana patsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paskha.

10. Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu.

11. Pamenepo anaphera Paskha; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.

12. Ndipo anacotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.

13. Ndipo anaoca Paskha pamoto, monga mwa ciweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.

14. Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 35