Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 35:20-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Citatha ici conse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aigupto anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Firate; ndipo Yosiya anamturukira kuyambana naye.

21. Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndiri ndi ciani ndi inu, mfumu ya Yuda? sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndiri nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kubvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.

22. Koma Yosiya sanatembenuka nkhope yace kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ocokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'cigwa ca Megido.

23. Ndipo oponya anayang'anitsa mibvi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ace, Ndicotseni ndalasidwa ndithu.

24. Pamenepo anyamata ace anamturutsa m'gareta, namuika m'gareta waciwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ace. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.

25. Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oyimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israyeli; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro.

26. Macitidwe ena tsono a Yosiya, ndi nchito zace zokoma, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova,

27. ndi zocita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 35