Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 34:31-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo mfumu inaimirira pokhala pace, nicita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda cotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, kucita mau a cipangano olembedwa m'bukumu.

32. Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anacita monga mwa cipangano ca Mulungu, Mulungu wa makolo ao.

33. Yosiya nacotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israyeli, natumikiritsa onse opezeka m'lsrayeli, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ace onse iwo sanapambuka kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 34