Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 34:27-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ace otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzicepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zobvala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.

28. Taona, ndidzakusonkhanitsa ku makolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.

29. Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akulu akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.

30. Nikwera mfumu ku nyumba ya Yehova ndi amuna onse a m'Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akuru ndi ang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.

31. Ndipo mfumu inaimirira pokhala pace, nicita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda cotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, kucita mau a cipangano olembedwa m'bukumu.

32. Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anacita monga mwa cipangano ca Mulungu, Mulungu wa makolo ao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 34