Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 33:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wace, nadzicepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ace.

13. Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwace, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wace. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.

14. Citatha ici tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'cigwa, mpaka polowera pa cipata cansomba; nazinga Ofeli, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.

15. Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.

16. Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israyeli.

17. Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.

18. Macitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lace kwa Mulungu wace, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli, taonani, zalembedwa m'niacitidwe a mafumu a Israyeli.

19. Pemphero lace lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi chimo lace lonse, ndi kulakwa kwace, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzicepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.

20. Momwemo Manase anagona ndi makolo ace, namuika m'nyumba mwace mwace; ndi Amoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

21. Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.

22. Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira Manase atate wace; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wace, nawatumikira.

23. Koma sanadzicepetsa pamaso pa Yehova, monga umo anadzicepetsera Manase atate wace; koma Amoni amene anacurukitsa kuparamula kwace.

24. Ndipo anyamata ace anampangira ciwembu, namupha m'nyumba yace yace.

25. Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira ciwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wace akhale mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 33