Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 33:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.

2. Nacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawacotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israyeli.

3. Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wace, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

4. Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa ku nthawi zonse.

5. Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehoya.

6. Anapititsanso ana ace pamoto m'cigwa ca ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.

7. Ndipo anaika cifanizo cosema ca fanolo adacipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomo mwana wace, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israyeli ndidzaika dzina langa ku nthawi zonse;

8. ndipo sindidzasunthanso phazi la Israyeli ku dziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kucita zonse ndawalamulira, cilamulo conse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.

9. Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.

10. Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ace, koma sanasamalira.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 33