Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 32:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Sanakeribu mfumu ya Asuri, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.

23. Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wace, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.

24. Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa cizindikilo codabwiza.

25. Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.

26. Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.

27. Ndipo cuma ndi ulemu zinacurukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golidi, ndi timiyala ta mtengo wace, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma ziri zonse;

28. ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iri yonse, ndi makola a zoweta.

29. Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zocuruka; pakuti Mulungu adampatsa cuma cambirimbiri.

30. Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire ku madzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo nchito zace zonse.

31. Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babulo, amene anatumiza kwa iye kufunsira za codabwiza cija cidacitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwace.

32. Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi nchito zace zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 32