Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 32:13-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Simudziwa kodi comwe ine ndi makolo anga tacitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?

14. Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga, kuti Mulungu wako adzakhoza kukulanditsa iwe m'dzanja mwanga?

15. Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe mulungu wa mtundu uli wonse wa anthu, kapena ufumu uli wonse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?

16. Ndipo anyamata ace anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wace Hezekiya,

17. Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ace m'dzanja mwanga.

18. Ndipo anapfuula ndi mau akuru m'cinenedwe ca Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwabvuta, kuti alande mudziwu.

19. Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo nchito ya manja a anthu.

20. Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ici, napfuulira Kumwamba.

21. Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, ku cigono ca mfumu ya Asuri. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi ku dziko lace. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wace, iwo oturuka m'matumbo mwace anamupha ndi lupanga pomwepo.

22. Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Sanakeribu mfumu ya Asuri, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.

23. Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wace, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.

24. Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa cizindikilo codabwiza.

25. Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.

26. Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 32