Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 30:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israyeli ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efraimu ndi Manase, kuti abwere ku nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha.

2. Pakuti mfumu idapangana ndi akuru ace, ndi msonkhano wonse wa m'Yerusalemu, kuti acite Paskha mwezi waciwiri.

3. Pakuti sanakhoza kumcita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikira, ndi anthu sadasonkhana ku Yerusalemu.

4. Ndipo cinthuci cinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.

5. Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israyeli lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikuru sanacita monga mudalembedwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 30