Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 29:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Hezekiya analowa ufumu wace ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Abiya mwana wa Zekariya.

2. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adacitira Davide kholo lace.

3. Caka coyamba ca ufumu wace, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.

4. Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamalo poyera kum'mawa,

5. nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kucotsa zoipsa m'malo opatulika.

6. Pakuti analakwa makolo athu, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya cokhalamo Yehova, namfulatira.

7. Anatsekanso pa khomo la likole, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israyeli.

8. Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale codabwiza ndi cotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu.

9. Pakuti taonani, makolo athu adagwa ndi lupanga, ndi ana athu amuna ndi akazi ndi akazi athu ali andende cifukwa ca ici.

10. Tsono mumtima mwanga nditi ndicite cipangano ndi Yehova Mulungu wa Israyeli, kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kuticokera.

11. Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pace, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ace ndi kufukiza zonunkhira.

12. Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoeli mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; ndi a Agerisoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;

13. ndi a ana a Elizafana, Simri ndi Yeueli; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya;

14. ndi a ana a Hemani, Yehudi ndi Simei ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyeli,

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 29