Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 28:10-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi mirandu yoparamula kwa Yehova Mulungu wanu?

11. Mundimvere tsono, bwezani andende amene munawatenga ndende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.

12. Pamenepo akuru ena a ana a Efraimu, Azariya mwana wa Yohanana, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo,

13. nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutiparamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa macimo athu ndi zoparamula zathu; pakuti taparamula kwakukuru, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israyeli.

14. Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga ndi msonkhano wonse.

15. Nanyamuka amuna ochulidwa maina, natenga andende, nabveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zobvala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofoka ao onse pa aburu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.

16. Nthawi yomweyi mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asuri amthandize.

17. Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.

18. Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kucidikha, ndi ya kumwela kwa Yuda, nalanda Betisemesi, ndi Azaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi miraga yace, ndi Timna ndi miraga yace; nakhala iwo komweko.

19. Pakuti Yehova anacepetsa Yuda cifukwa ca Ahazi mfumu ya Israyeli; popeza iye anacita comasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.

20. Ndipo Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.

21. Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asuri, osathandizidwa nazo.

22. Ndipo nthawi ya nsautso yace anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.

23. Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisrayeli onse.

24. Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngondya ziri zonse za Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 28