Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 25:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yace, naigwadira, naifukizira,

15. Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?

16. Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwacita ici ndi kusamvera kupangira kwanga.

17. Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani, tionane maso.

18. Ndi Yoasi mfumu ya Israyeli anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebano inapitapo, nipondereza mtungwi.

19. Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.

20. Koma wosamvera Amaziya, pakuti nca Mulungu ici kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 25