Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 25:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Yehoadana wa ku Yerusalemu.

2. Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosacita ndi mtima wangwiro.

3. Kunacitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ace amene adapha mfumu atate wace.

4. Koma sanapha ana ao, koma anacita monga umo mulembedwa m'cilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere chimo lace lace.

5. Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akuturukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi cikopa.

6. Analemberanso ngwazi zamphamvu za m'Israyeli zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente a siliva zana limodzi.

7. Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israyeli lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israyeli, sakhala ndi ana onse a Efraimu.

8. Koma ngati mumuka, citani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.

9. Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.

10. Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kucokera ku Efraimu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.

11. Nalimbika mtima Amaziya, natsogolera anthu ace, namuka ku Cigwa ca Mcere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.

12. Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, nawakankha pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 25