Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 23:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi maraya acitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba, ya Mulungu.

10. Ndipo anaika anthu onse, yense ndi cida cace m'dzanja lace, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya ku dzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya ku dzanja lamanzere la nyumba, kuloza ku guwa la nsembe ndi kunyumba.

11. Pamenepo anaturutsa mwana wa mfumu, nambveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ace anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.

12. Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;

13. napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yace polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oyimbira omwe analiko ndi zoyimbirazo, nalangiza poyimbira colemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, nati, Ciwembu, ciwembu.

14. Koma Yehoyada wansembe anaturuka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mturutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo ali yense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.

15. Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku cipata ca akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 23