Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 22:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nabwerera iye kuti amcize ku Yezreeli, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaeli mfumu ya Aramu, Ndipo Azariya mwana wa Yehoramu mfumu yaYuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, popeza anadwala.

7. Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehocamu; pakuti atafika anaturukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimsi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

8. Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Israyeli, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.

9. Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wace wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.

10. Pamene Ataliya anaona kuti mwana wace adafa, anauka, naononga mbeu yonse yacifumu ya nyumba ya Yuda.

11. Koma Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wace m'cipinda cogonamo. Momwemo Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wace wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.

12. Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi cimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 22