Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 22:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wace wamng'ono akhale mfumu m'malo mwace; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kucigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda.

2. Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Ataliya mwana wa Omri.

3. Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi mace acite coipa,

4. Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wace; ndi kuonongeka kwace nkumeneko.

5. Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, kukayambana nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

6. Nabwerera iye kuti amcize ku Yezreeli, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaeli mfumu ya Aramu, Ndipo Azariya mwana wa Yehoramu mfumu yaYuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, popeza anadwala.

7. Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehocamu; pakuti atafika anaturukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimsi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

8. Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Israyeli, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.

9. Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wace wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 22