Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 21:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, umo anacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wace; ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova.

7. Koma Yehova sanafuna kuononga nyumba ya Davide cifukwa ca pangano adalicita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ace nyali nthawi zonse.

8. Masiku ace Aedomu anapanduka kucoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.

9. Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ace, ndi magareta ace onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magareta,

10. Cinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lace; cifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ace.

11. Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nacititsa okhala m'Yerusalemu cigololo, nakankhirako Ayuda.

12. Ndipo anamdzera kalata wofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayenda m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,

13. koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, ndi kucititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu cigololo, monga umo anacitira cigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 21