Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 20:13-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Ayuda onse anakhala ciriri pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.

14. Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahazieli mwana wa Zekriya, mwana wa Benaya, mwana wa Yetieli, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano;

15. nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa cifukwa ca aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.

16. Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera cigwa cakuno ca cipululu ca Yerueli.

17. Si kwanu kucita nkhondo kuno ai; cirimikani, imani, nimupenye cipulumutso ca Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwaturukire, popeza Yehova ali ndi inu.

18. Ndipo Yehosafati anawerama mutu wace, nkhope yace pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.

19. Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mau omveketsa.

20. Nalawira mamawa, naturuka kumka ku cipululu ca Tekoa; ndipo poturuka iwo, Yehosafati anakhala ciriri, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, Hmbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ace, ndipo mudzalemerera.

21. Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza ciyero cokometsetsa, pakuturuka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cosatha.

22. Ndipo poyamba iwo kuyimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.

23. Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.

24. Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.

25. Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka.

26. Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino.

27. Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.

28. Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, ku nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 20