Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 2:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala Ralo, luntha, Huramu Abi,

14. ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wace ndiye munthu wa ku Turo, wodziwa kucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira copanga ciri conse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.

15. Ndipo tsono tirigu ndi barele, mafuta ndi vinyo, mbuye wanga wanenazi, azitumize kwa anyamata ace;

16. ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebano monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

17. Ndipo Solomo anawerenga alendo Onse okhala m'dziko la Israyeli, monga mwa mawerengedwe aja atate wace Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.

18. Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndilimodzi agwiritse anthu nchito.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 2