Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 19:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, m'mudzi m'mudzi;

6. nati kwa oweruza, Khalani maso umo mucitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

7. Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kucita; pakuti palibe cosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.

8. Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli, aweruzire Yehova, nanene mirandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.

9. Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 19