Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 14:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. nacotsa maguwa a nsembe acilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,

4. nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kucita cilamulo ndi cowauza, Iye.

5. Anacotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unacita bata pamaso pace.

6. Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7. Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosabvutika.

8. Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.

9. Ndipo anawaturukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi cikwi cimodzi, ndi magareta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

10. Naturuka Asa pamaso pace, nanika nkhondoyi m'cigwa ca Sefata ku Maresa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 14