Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 14:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Momwemo Abiya anagona ndi makolo ace, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, m'masiku ace dziko linaona bata zaka khumi.

2. Ndipo Asa anacita cokoma ndi coyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wace,

3. nacotsa maguwa a nsembe acilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,

4. nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kucita cilamulo ndi cowauza, Iye.

5. Anacotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unacita bata pamaso pace.

6. Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7. Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosabvutika.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 14