Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 11:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ocokera m'mafuko onse a Israyeli, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.

17. Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehabiamu, mwana wa Solomo zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomo zaka zitatu.

18. Ndipo Rehabiamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliabu mwana wa Jese;

19. ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.

20. Ndi pambuyo pace anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.

21. Ndipo Rehabiamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ace onse, ndi akazi ace ang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi ang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana akazi makumi asanu ndi limodzi).

22. Ndipo Rehabiamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkuru, kalonga mwa abale ace; ndiko kuti adzamlonga ufumu.

23. Ndipo anacita mwanzeru, nabalalitsa ana ace amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, ku midzi yonse yamalinga; nawapatsa cakudya cocuruka, nawafunira akazi ocuruka.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 11