Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 11:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndi m'midzi iri yonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa cilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ace.

13. Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israyeli lonse anadziphatikiza kwa iye, ocokera m'malire ao Onse.

14. Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko ao ao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobiamu ndi ana ace anawataya, kuti asacitire Yehova nchito ya nsembe;

15. nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a ana a ng'ombe adawapanga.

16. Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ocokera m'mafuko onse a Israyeli, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.

17. Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehabiamu, mwana wa Solomo zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomo zaka zitatu.

18. Ndipo Rehabiamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliabu mwana wa Jese;

19. ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 11