Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 10:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.

11. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12. Tsono Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.

13. Ndipo mfumu inawayankha mokaripa, popeza mfumu Rehabiamu analeka uphungu wa akulu akulu,

14. nalankhula nao monga umo anampangira acinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

15. Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ace, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.

16. Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu, Aisrayeli inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisrayeli onse anamuka ku mahema ao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 10