Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 10:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Rehabiamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisrayeli onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2. Ndipo kunali, atamva Yerobiamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Aigupto kumene adathawira, kuthawa Solomo mfumu), Yerobiamu anabwera kucoka ku Aigupto.

3. Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobiamu ndi Aisrayeli onse, nalankhula ndi Rehabiamu, ndi kuti,

4. Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko nchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lace lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.

5. Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nacoka anthu.

6. Ndipo Rehabiamu mfumu anafunsana ndi akulu akulu, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?

7. Ndipo ananena naye, kuti, Mukawacitira cokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.

8. Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 10