Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 9:25-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wace, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezreeli; pakuti kumbukila m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wace, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.

26. Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ace, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova, Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.

27. Koma pociona ici Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku khumbi la m'munda. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagareta; namkantha pa cikweza ca Guru ciri pafupi pa Yibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.

28. Ndipo anyamata ace anamnyamulira pagareta kumka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ace pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

29. Ndipo pa caka cakhumi ndi cimodzi ca Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.

30. Ndipo pofika Yehu ku Yezreeli, Yezebeli anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lace, nasuzumira pazenera.

31. Ndipo polowa Yehu pacipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimri, iwe wakupha mbuyako?

32. Koma anakweza maso ace kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.

33. Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wace pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.

34. Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

35. Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezako kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.

36. Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananena wo mwa mtumiki wace Eliya wa ku Tisibe, ndi koti, Pa munda wa Yezreeli agaru adzadya mnofu wa Yezebeli;

37. ndi thupi la Yezebeli lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezreeli, kuti sadzati, Ndi Yezebeli uyu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 9