Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 8:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pamenepo Yoramu anaoloka kumka ku Zairi, ndi magareta ace onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magareta, nathawira anthu ku mahema ao.

22. Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.

23. Ndi macitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazicita, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda.

24. Nagona Yoramu ndi makolo ace, naikidwa pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

25. Caka cakhumi ndi ziwiri ca Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

26. Ahaziya ndiye, Wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi. Ndi dzina la mace ndiye Ataliya mdzukulu wa Omri mfumu ya Israyeli.

27. Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nacita coipa pamaso pa Yehova, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa cibale ca banja la Ahabu.

28. Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.

29. Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezreeli mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu, Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, pakuti anadwala.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 8