Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wace, Nditengere cotengera cina, Nanena naye, Palibe cotengera cina. Ndipo mafuta analeka.

7. Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.

8. Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kumka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyu, adafowapa, mbukirako kukadya mkate.

9. Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wace, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano cipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu.

10. Timmangire kacipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi coikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo.

11. Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'cipinda cosanja, nagona komweko.

12. Nati kwa Gehazi mnyamata wace, Itana Msunemu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pace.

13. Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikucitire iwe ciani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4