Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:33-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.

34. Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pace ndi pakamwa pace, maso ace ndi maso ace, zikhato zace ndi zikhato zace, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35. Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, cakuno kamodzi, cauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ace.

36. Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunemu uja, Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ace, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wace, naturuka.

38. Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pace; ndipo anati kwa mnyamata wace, Ika nkhali yaikuruyo, uphikire ana a aneneri.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4