Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:20-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Namnyamula, napita naye kwa amace. Ndipo anakhala pa maondo ace kufikira usana, namwalira.

21. Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, naturuka, namtsekera.

22. Naitana mwamuna wace, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi buru mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

23. Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero cifukwa ninji? ngati mwezi wakhala, kapena: mpa sabata? Koma anati, Kuli bwino.

24. Pamenepo anamangirira buru mbereko, nati kwa mnyamata wace, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

25. Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu ku phiri la Karimeli. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wace, Tapenya, suyo Msunemu uja;

26. uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? mwamuna wanu ali bwino? mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

27. Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wace ulikumwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ici.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4