Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamenepo anati, Nanga timcitire iye ciani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wace wakalamba.

15. Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.

16. Ndipo anati, Nyengo yino caka cikudzaci udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, lai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.

17. Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo caka cimene cija Elisa adanena naye.

18. Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anaturuka kumka kwa atate wace, ali kwa omweta tirigu.

19. Natikwa atate wace, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amace.

20. Namnyamula, napita naye kwa amace. Ndipo anakhala pa maondo ace kufikira usana, namwalira.

21. Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, naturuka, namtsekera.

22. Naitana mwamuna wace, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi buru mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

23. Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero cifukwa ninji? ngati mwezi wakhala, kapena: mpa sabata? Koma anati, Kuli bwino.

24. Pamenepo anamangirira buru mbereko, nati kwa mnyamata wace, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

25. Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu ku phiri la Karimeli. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wace, Tapenya, suyo Msunemu uja;

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4