Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 25:25-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Koma kunali mwezi wacisanu ndi ciwiri anadza Ismayeli mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yacifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Akasidi okhala naye ku Mizipa.

26. Pamenepo ananyamuka anthu onse ang'ono ndi akuru, ndi akazembe a makamu, nadza ku Aigupto; pakuti anaopa Akasidi.

27. Ndipo kunali caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri ca kumtenga ndende Yoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili Merodaki mfumu ya Babulo anamuweramutsa mutu wace wa Yoyakini mfumu ya Yuda aturuke m'kaidi, caka colowa iye ufumu wace;

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 25