Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 25:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iye ndi khamu lace lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.

2. Ndipo mudziwo unazingidwa ndi timalinga mpaka caka cakhumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.

3. Tsiku lacisanu ndi cinai la mwezi wacinai njala idakula m'mudzimo, panalibe cakudya kwa anthu a m'dzikomo.

4. Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku cipata ca pakati pa makoma awiri, iri ku munda wa mfumu; Akasidi tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kucidikha.

5. Koma nkhondo ya Akastdi inalondola mfumu, niipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yace yonse inambalalikira.

6. Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babulo ku Ribila, naweruza mlandu wace.

7. Napha ana a Zedekiya pamaso pace, namkolowola Zedekiya maso ace, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka nave ku Babulo.

8. Ndipo mwezi wacisanu, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo, ndico caka cakhumi mphambu cisanu ndi cinai ca mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babulo, Nebuzaradani mkuru wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babulo, anadza ku Yerusalemu,

9. natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikuru anazitentha ndi moto.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 25