Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku cipata ca pakati pa makoma awiri, iri ku munda wa mfumu; Akasidi tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kucidikha.