Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nagamula nyumba za anyamata adama okhala ku nyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsaru zolenjeka za cifanizoco.

8. Naturutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa cipata ca Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa cipata ca mudzi.

9. Koma ansembe a misanje sanakwera kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda cotupitsa pakati pa abale ao.

10. Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'cigwa ca ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wace wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.

11. Nacotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku cipinda ca Natani Meleki mdindoyo, cokhala kukhonde; natentha magareta a dzuwa ndi moto.

12. Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa cipinda cosanja ca Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwacotsa komweko, nitaya pfumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.

13. Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la cionongeko, imene Solomo mfumu ya Israyeli adaimangira Asitoreti conyansa ca Asidoni, ndi Kemosi conyansa ca Moabu, ndi Milikomu conyansa ca ana a Amoni.

14. Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23