Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.

7. Nagamula nyumba za anyamata adama okhala ku nyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsaru zolenjeka za cifanizoco.

8. Naturutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa cipata ca Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa cipata ca mudzi.

9. Koma ansembe a misanje sanakwera kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda cotupitsa pakati pa abale ao.

10. Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'cigwa ca ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wace wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23