Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:33-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo Faraoneko anammanga m'Ribila, m'dziko la Hamati; kuti asacite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golidi.

34. Ndipo Farao-Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wace, nasanduliza dzina lace likhale Yoyakimu; koma anapita naye Yoahazi, nafika iye m'Aigupto, nafa komweko.

35. Ndipo Yoyakimu anapereka siliva ndi golidi kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golidi, yense monga mwa kuyesedwa kwace, kuzipereka kwa Farao-Neko.

36. Yoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.

37. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita makolo ace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23