Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndi nyumba zonse zoo mwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israyeli kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazicotsa, nazicitira monga mwa nchito zonse adazicita ku Beteli.

20. Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha-mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kumka ku Yerusalemu.

21. Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mcitireni Yehova Mulungu wanu Paskha, monga mulembedwa m'buku ili la cipangano,

22. Zedi silinacitika Paskha lotere ciyambire masiku a oweruza anaweruza Israyeli, ngakhale m'masiku a mafumu a Israyeli, kapena mafumu a Yuda;

23. koma Paskha ili analicitira Yehova m'Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.

24. Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazicotsa; kuti alimbitse mau a cilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.

25. Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, ndi mphamvu yace yonse, monga mwa cilamulo conse ca Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.

26. Koma Yehova sanakululuka mkwiyo wace waukuru waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, cifukwa ca zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23