Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa cipinda cosanja ca Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwacotsa komweko, nitaya pfumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.

13. Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la cionongeko, imene Solomo mfumu ya Israyeli adaimangira Asitoreti conyansa ca Asidoni, ndi Kemosi conyansa ca Moabu, ndi Milikomu conyansa ca ana a Amoni.

14. Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.

15. Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Beteli, ndi msanje adaumanga Yerobiamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israyeli uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale pfumbi, natentha cifanizoco.

16. Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu naturutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23